Publicidade

1 João 2

12 Inu ana okondedwa, ndikukulemberani

popeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu.

13 Inu abambo, ndikukulemberani

popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.

Inu anyamata, ndikukulemberani

popeza kuti munagonjetsa woyipayo.

14 Ana okondedwa, ndikukulemberani

chifukwa mumawadziwa Atate.

Abambo, ndikukulemberani

chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.

Inu anyamata, ndikukulemberani

chifukwa ndinu amphamvu.

Mawu a Mulungu amakhala mwa inu

ndipo mumamugonjetsa woyipayo.

Musakonde Dziko Lapansi

15 Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate.

Veja também

Publicidade
1 João
Ver todos os capítulos de 1 João
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-22_10-02-25-