Mulungu ndiye Chikondi
7 Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu. 8 Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.