23 Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. 24 Pakuti,
"Anthu onse ali ngati udzu,
ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo.
Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,
25 koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya."
Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.