Akazi ndi Amuna
1 Momwemonso, akazi inu gonjerani amuna anu kuti ngati ena a iwo sakhulupirira Mawu a Mulungu, akopeke ndi makhalidwe a akazi awo ndipo sipadzafunikanso mawu 2 pamene aona moyo wanu wachiyero ndi moyo woopa Mulungu. 3 Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere. 4 Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu. 5 Pakuti umo ndi mmene akazi oyera mtima akale amene anali ndi chiyembekezo pa Mulungu anadzikongoletsera. Iwo ankagonjera amuna awo, 6 monga Sara, amene anamvera Abrahamu namutcha iye mbuye wake. Akazi inu ndinu ana ake ngati muchita zoyenera, ndipo musaope choopsa chilichonse.