2 Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu. 3 Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa. 4 Anthu osapembedza amadabwa pamene simuthamangira nawo kuchita zoyipitsitsazi, nʼchifukwa chake amakuchitani chipongwe. 5 Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. 6 Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu.
7 Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera.