8 Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. 9 Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
10 Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba.