36 Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, "Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu. 37 Ndiyankheni, Inu Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe Inu Yehova, kuti ndinu Mulungu, ndipo kuti mutembenuziranso mitima yawo kwa Inu."
38 Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhuni, miyala ndi dothi lomwe. Unawumitsanso madzi amene anali mʼngalande.
39 Anthu onse ataona zimenezi, anaweramitsa nkhope zawo pansi, nafuwula kuti, "Yehova ndiye Mulungu! Yehova ndiye Mulungu!"