41 Ndipo Eliya anati kwa Ahabu, "Pitani, kadyeni ndi kumwa, pakuti kukumveka mkokomo wa mvula." 42 Choncho Ahabu anapita kukadya ndi kumwa, koma Eliya anakwera pamwamba pa Phiri la Karimeli, ndipo anawerama mpaka pansi, nayika mutu wake pakati pa mawondo ake.
43 Eliya anawuza mtumiki wake kuti, "Pita kayangʼane ku nyanja." Ndipo iye anapita nakayangʼana.
Mtumikiyo anati, "Kulibe kanthu."
Kasanu nʼkawiri Eliya anati, "Pitanso."
44 Ulendo wachisanu ndi chiwiri mtumikiyo anafotokoza kuti, "Taonani, kamtambo kakangʼono kokhala ngati dzanja la munthu kakutuluka ku nyanja."
Pamenepo Eliya anati, "Pita, kamuwuze Ahabu kuti, ‘Konzani galeta lanu ndipo mutsike mvula isanakutsekerezeni.’ "
45 Nthawi imeneyi nʼkuti kuthambo kutayamba kusonkhana mitambo yakuda, mphepo inawomba, mvula yamphamvu inagwa ndipo Ahabu anakwera galeta napita ku Yezireeli.