Eliya Athawira ku Phiri la Horebu
1 Tsono Ahabu anawuza Yezebeli zonse zimene anachita Eliya ndi momwe anaphera aneneri onse ndi lupanga. 2 Choncho Yezebeli anatuma mthenga kwa Eliya kuti akamuwuze kuti, "Milungu indilange, ndipo indilange koopsa, ngati mawa nthawi ngati yomwe ino sindidzakupha iwe monga unaphera aneneriwo."
3 Eliya ataona zimenezi, ananyamuka nathawa kupulumutsa moyo wake. Atafika ku Beeriseba ku Yuda, anasiya mtumiki wake kumeneko, 4 ndipo Eliyayo anayenda ulendo wa tsiku limodzi mʼchipululu. Anafika pa kamtengo ka tsache, nakhala pansi pa tsinde lake napemphera kuti afe. Iye anati, "Yehova, ine ndatopa nazo. Chotsani moyo wanga. Ineyo sindine wopambana makolo anga." 5 Ndipo Eliya anagona tulo tofa nato pa tsinde pa kamtengoko.
Ndipo taonani, mngelo anamukhudza, namuwuza kuti, "Dzuka udye." 6 Eliya anayangʼana, ndipo taonani kumutu kwake kunali buledi wootcha pa makala ndi botolo la madzi. Iye anadya ndi kumwa, nʼkugonanso.
7 Mngelo wa Yehova anabweranso kachiwiri, anamukhudza, namuwuza kuti, "Dzuka udye, popeza ulendowu ndi wautali." 8 Tsono Eliya anadzuka nadya ndi kumwa. Atapeza mphamvu chifukwa cha chakudyacho, anayenda masiku 40, usana ndi usiku mpaka anafika ku Horebu, phiri la Mulungu.