Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Reis 19

20 Pomwepo Elisa anasiya ngʼombe zake nathamangira Eliya. Iye anati, "Mundilole kuti ndikatsanzike abambo ndi amayi anga, ndipo kenaka ndidzakutsatani."

Eliya anayankha kuti, "Bwerera. Ine ndachita chiyani kwa iwe?"

21 Choncho Elisa anamusiya Eliyayo nabwerera kwawo. Anatenga ngʼombe zake ziwiri zapagoli nazipha. Anatenga magoli a mapulawo ake nasonkhera moto kuphikira nyamayo ndipo anayipereka kwa anthu kuti adye. Ndipo ananyamuka natsatira Eliya ndi kukhala mtumiki wake.

Veja também