5 Ndipo Eliya anagona tulo tofa nato pa tsinde pa kamtengoko.
Ndipo taonani, mngelo anamukhudza, namuwuza kuti, "Dzuka udye." 6 Eliya anayangʼana, ndipo taonani kumutu kwake kunali buledi wootcha pa makala ndi botolo la madzi. Iye anadya ndi kumwa, nʼkugonanso.