Publicidade

1 Reis 3

5 Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, "Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa."

6 Solomoni anayankha kuti, "Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.

7 "Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi. 8 Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga. 9 Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?"

10 Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi. 11 Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, "Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, 12 Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako.

Veja também

Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-04_23-13-58-