13 Mfumu Solomoni inasonkhanitsa anthu ogwira ntchito ya thangata mʼdziko lonse la Israeli ndipo anthu athangatawo analipo 30,000. 14 Iye ankatumiza anthu 10,000 ku Lebanoni pa mwezi mosinthanasinthana, kotero kuti ankakhala ku Lebanoniko mwezi umodzi ndipo kwawo ankakhalako miyezi iwiri. Adoniramu ndiye ankayangʼanira ogwira ntchito yathangatayo. 15 Solomoni anali ndi anthu amtengatenga 70,000, anthu 80,000 osema miyala ku mapiri, 16 ndi akapitawo 33,000 amene ankayangʼanira ntchitoyi ndiponso anthu ogwira ntchito zina.