10 Hana anavutika mʼmoyo mwake, ndipo anapemphera kwa Yehova akulira kwambiri. 11 Ndipo iye analumbira kuti, "Inu Yehova Wamphamvuzonse, ngati muyangʼana kusauka kwa mtumiki wanune, ndi kuyankha pemphero langa osandiyiwala ine mtumiki wanu pondipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzamupereka mwanayo kwa inu Yehova masiku onse a moyo wake. Lumo silidzapita pa mutu pake."
15 Koma Hana anayankha kuti, "Sichoncho mbuye wanga. Ndakhala ndikumukhuthulira Yehova chisoni changa. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa chilichonse, popeza nthawi yonseyi ndakhala ndikupereka kwa Yehova nkhawa yayikulu ndi mavuto anga.
17 Eli anayankha, "Pitani mu mtendere, ndipo Mulungu wa Israeli akupatseni zimene mwamupemphazo."
20 Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, "Ndinachita kumupempha kwa Yehova."