22 Koma Hana sanapite nawo popeza anawuza mwamuna wake kuti, "Mwanayu akadzaleka kuyamwa, ndidzapita naye ndi kukamupereka pamaso pa Yehova ndipo adzakhala kumeneko moyo wake wonse."
23 Elikana mwamuna wake anamuwuza kuti, "Chita chimene chakukomera. Tsala kuno mpaka utamusiyitsa kuyamwa, Yehova yekha akwaniritse mawu ake." Choncho mkaziyo anatsala ku nyumba ndi kusamalira mwana wake mpaka atamuletsa kuyamwa.
24 Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo.