11 Samueli anafunsa kuti, "Nʼchiyani chimene wachita?"
Sauli anayankha kuti, "Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi, 12 ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, chonsecho sindinapemphe Yehova kuti andikomere mtima.’ Motero ndinakakamizika kupereka nsembe yopsereza."