11 Usiku womwewo Sauli anatumiza anthu ku nyumba ya Davide kuti akamubisalire ndi kumupha mmamawa. Koma Mikala mkazi wake anamuchenjeza nati, "Ngati usiku uno supulumutsa moyo wako, mawa udzaphedwa." 12 Choncho Mikala anamutulutsira Davide pa zenera, ndipo anathawa ndi kupulumuka. 13 Kenaka Mikala anatenga fano naligoneka pa bedi nayika pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwa fanolo ndipo analifunditsa nsalu.
14 Pamene amithenga a Sauli aja anafika kuti akamugwire Davide, Mikala anati, "Davide akudwala."
15 Koma Sauli anatumanso anthuwo kuti akamuone Davide, nati, "Mubwere naye kuno ali pa bedi pomwepo kuti ndidzamuphe." 16 Koma pamene anthuwo analowa, anangoona fano pa bedipo ndi pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwake.
17 Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, "Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?"
Mikala anayankha kuti, "Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’ "
18 Choncho Davide anathawa napulumuka. Pambuyo pake anapita kwa Samueli ku Rama nakamuwuza zonse zimene Sauli anamuchita. Kenaka iye ndi Samueli anapita kukakhala ku Nayoti.