Pular para o conteúdo
Publicidade

1 SAMUELI 2

Pemphero la Hana

1 Ndipo Hana anapemphera nati,

"Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova;

Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova.

Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola.

Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa.

2 "Palibe wina woyera ngati Yehova,

palibe wina koma inu nokha,

palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.

3 "Musandiyankhulenso modzitama,

pakamwa panu pasatuluke zonyada,

pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru,

ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.

4 "Mauta a anthu ankhondo athyoka

koma anthu ofowoka avala dzilimbe.

5 Amene kale anali okhuta tsopano akukagula chakudya,

koma iwo amene anali ndi njala sakumvanso njala.

Amene anali wosabereka, wabereka ana aamuna asanu ndi awiri,

koma iye wobereka ana ambiri watsala yekha.

6 "Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo,

amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso.

7 Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa,

amatsitsa ndipo amakweza.

8 Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi,

ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala.

Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu,

amawapatsa mpando waulemu.

"Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova,

anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.

9 Iye adzateteza moyo wa anthu okhulupirika

koma anthu oyipa adzawonongedwa mu mdima.

"Pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake.

10 Yehova adzaphwanya omutsutsa.

Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba;

Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi.

"Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake,

adzakuza mphamvu za odzozedwa wake."

Veja também