Kuyipa kwa Ana a Eli
12 Ana a Eli anali ana achabechabe pakuti samasamala za Yehova. 13 Ndipo chizolowezi cha ansembe pakati pa anthu chinali motere kuti pamene munthu aliyense ankapereka nsembe ndipo nyama ija ikuwira pa moto, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi chifoloko cha mano atatu mʼdzanja lake. 14 Iye ankachipisa mu mʼphikamo, ndipo wansembeyo amatenga chilichonse chimene folokoyo yabaya. Umu ndi mmene ansembewo amachitira ndi Aisraeli onse amene amabwera ku Silo. 15 Ndipo ngakhale mafuta asanatenthedwe, mtumiki wansembe amabwera ndi kunena kwa munthu amene akupereka nsembeyo kuti, "Ndipatse nyama kuti ndiwotche, pakuti Yehova salandira nyama yophika koma yayiwisi."
16 Ngati munthuyo anena kuti, "Apseretu mafuta poyamba, ndipo kenaka mutenge mmene mufunira," mtumikiyo amayankha kuti, "Ayi ndipatse tsopano lino. Ngati sutero, ine nditenga molanda."
17 Tchimo la ana a Eli linali lalikulu kwambiri pamaso pa Yehova pakuti iwo amanyoza nsembe za Yehova.