Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Samuel 20

41 Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri.

42 Yonatani anawuza Davide kuti, "Pita mu mtendere pakuti ife awiri tinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, Yehova ndiye akhale mboni pakati pa iwe ndi ine ndiponso pakati pa zidzukulu zako ndi zidzukulu zanga kwa nthawi yonse.’ " Kenaka Davide anachoka, ndipo Yonatani anabwerera ku mzinda kuja.

Veja também