7 Kenaka Sauli anawuza nduna zake kuti, "Mundipezere mkazi amene amawombeza mawula kuti ndipite ndikafunse kwa iye."
Nduna zakezo zinamuyankha kuti, "Alipo mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ku Endori."
15 Samueli anafunsa Sauli kuti, "Nʼchifukwa chiyani wandivutitsa pondiyitana kuti ndibwere kuno?"
Sauli anayankha kuti, "Ine ndavutika kwambiri mʼmaloto. Afilisti akumenyana nane, ndipo Mulungu wandifulatira. Iye sakundiyankhulanso, ngakhale kudzera mwa aneneri kapena maloto. Choncho ndakuyitanani kuti mundiwuze zoti ndichite."