Yehova Ayitana Samueli
1 Samueli ankatumikira Yehova moyangʼaniridwa ndi Eli. Masiku amenewo mawu a Yehova sankamveka pafupipafupi. Kuona zinthu mʼmasomphenya sikunkachitikanso kawirikawiri.
4 Yehova anayitana Samueli.
Iye anayankha kuti, "Wawa." 5 Ndipo iyeyo anathamangira kwa Eli ndipo anati, "Ndabwera ndamva kuyitana."
Koma Eli anati, "Ine sindinakuyitane, bwerera kagone." Ndipo iye anapita kukagona.
6 Yehova anayitananso, "Samueli!" Ndipo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli nati, "Ndabwera popeza ndamva mukundiyitana."
Eli nati, "Mwana wanga, ine sindinakuyitane, bwerera kagone."
7 Nthawiyi nʼkuti Samueli asanadziwe Yehova ndipo Mawu a Yehova nʼkuti asanawululidwe kwa iye.
8 Yehova anayitananso Samueli kachitatu ndipo Samueli anadzuka ndikupita kwa Eli ndipo anati, "Ndabwera popeza mwandiyitana ndithu."
Apo Eli anazindikira kuti Yehova ndiye ankayitana mnyamatayo. 9 Tsono Eli anamuwuza Samueli kuti, "Pita ukagone ndipo akakuyitananso ukanene kuti, ‘Yankhulani Yehova, pakuti mtumiki wanu ndikumvetsera.’ " Choncho Samueli anapita ndi kukagona pamalo pake.
10 Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, "Samueli! Samueli!"
Ndipo Samueli anayankha, "Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera."