Publicidade

1 Samuel 6

Bokosi la Chipangano Libwerera ku Israeli

1 Bokosi la Yehova linakhala mʼdziko la Afilisti kwa miyezi isanu ndi iwiri. 2 Tsono Afilisti anayitana ansembe ndi amawula ndipo anati, "Tichite nalo chiyani Bokosi la Yehova? Tiwuzeni momwe tidzalitumizira ku malo ake."

3 Iwo anayankha kuti, "Ngati mufuna kubweza Bokosi la Mulungu wa Israeli, musalitumize wopanda kanthu, koma muyesetse kulitumiza pamodzi ndi nsembe yopepesera machimo. Mukatero mudzachiritsidwa, ndipo mudzadziwa chifukwa chiyani chilango cha Yehova sichikukuchokani."

Veja também

Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_12-11-46-