Zowayenereza Oyangʼanira ndi Atumiki
1 Mawu woona ndi awa: Ngati munthu akufunitsitsa atakhala woyangʼanira, ndiye kuti akufuna ntchito yabwino. 2 Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa. 3 Asakhale chidakwa, asakhale wandewu, koma wofatsa, asakhale wokonda mikangano, kapena wokonda ndalama. 4 Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni. 5 (Ngati munthu sadziwa kusamala banja lake lomwe, angathe bwanji kusamala mpingo wa Mulungu?) 6 Asakhale wongotembenuka mtima kumene kuopa kuti angadzitukumule napezeka pa chilango monga Satana. 7 Ayeneranso kukhala munthu wambiri yabwino ndi akunja, kuti anthu asamutonze nagwa mu msampha wa Satana.