16 Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. 17 Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya.
Publicidade
Publicidade