3 Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; 4 aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, 5 osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu. 6 Pa zimenezi munthu asachimwire mʼbale wake kapena kumuonerera. Ambuye adzalanga anthu onse amene amachita machimo amenewa, monga tinakuwuzani kale ndi kukuchenjezani. 7 Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima.
Publicidade
Publicidade