Pular para o conteúdo
Publicidade

1 ATESALONIKA 5

Tsiku la Ambuye

1 Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni, 2 chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku. 3 Pamene anthu akunena kuti, "Mtendere ndi chitetezo," chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.

4 Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. 5 Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também

1 Tessalonicenses
Ver todos os capítulos de 1 Tessalonicenses