14 Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino. 15 Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka. 16 Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi? 17 Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.
2 Akorinto 2:14-17
Em outras traduções
- NTNYBL2025 Nyanja
14 Nambho wayamikidwe Mnungu uyo watichogoza kukhoza kwa kulunjana ni Kilisito. Iye watichita tieneze uzene wa Kilisito ngati mnunghilo wa bwino kila kumalo. 15 Pakuti ife tilingati mnunghilo wa bwino wa Kilisito pamaso pa Mnungu, uwo wafikila wandhu wonjhe, yao amkhulupilila Kilisito ni wandhu yawo sadamkhulupilile Kilisito. 16 Kwaanyiyao amkhulupilila Kilisito, mnunghilo umeneo ni umoyo, nambho kwa anyiyao sadamkhulupilile Kilisito, mnunghilo umeneo ni nyifa. Yani uyo wakhoza kuchita njhito ya mtundu umeneo? 17 Ife osati ngati wina yao achita malonda ya Uthenga wa Mnungu, nambho tilalikila uzene pamaso pa Mnungu, ngati wandhu yao tatumidwa ni Mnungu uku tili olunjana ni Kilisito.
Direitos das traduções citadas
Estes versículos te tocaram? Ore agora!
+581 estão orando agora.
Junte-se à corrente de oração.