Publicidade

2 Coríntios 5

17 Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano. 18 Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. 19 Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso. 20 Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21 Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-