4 Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. 5 Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; 6 pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi 7 ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. 8 Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza. 9 Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa. 10 Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.