Kulimbikitsa Zopereka
1 Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. 2 Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. 3 Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, 4 ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. 5 Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu.