12 Yehova anamuonekera usiku ndipo anati:
"Ine ndamva pemphero lako ndipo ndadzisankhira malo ano kukhala Nyumba yanga yoperekeramo nsembe.
13 "Ine ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe, kapena kulamulira dzombe kuti liwononge dziko, kapena kutumiza mliri pakati pa anthu, 14 ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo.