Pular para o conteúdo
Publicidade

2 Mbiri 9:1-8

Mfumu Yayikazi ya ku Seba Ichezera Solomoni

1 Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni, inabwera mu Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. Inafika ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri, ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake. 2 Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta kwa iye komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo. 3 Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru za Solomoni komanso nyumba yaufumu imene anamanga, 4 chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo; atumiki opereka zakumwa ndi zovala zawo ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.

5 Iyo inati kwa mfumu, "Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu, ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona. 6 Koma sindinakhulupirire zimene ankanena mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe la kuchuluka kwa nzeru zanu, pakuti zaposa zimene ndinamva. 7 Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu! 8 Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando wake waufumu kuti mulamulire mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa cha chikondi cha Mulungu wanu pa Israeli, ndi khumbo lake kuti akusungeni mpaka muyaya, Iye wayika inu kukhala mfumu yawo kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.