Kuchiritsidwa kwa Madzi
19 Anthu a mu mzindamo anati kwa Elisa, "Mbuye wathu, taonani mzinda uno uli pamalo pabwino, monga mukuoneramu, koma madzi ake ndi oyipa, nthaka yakenso ndi yosabereka."
20 Iye anati, "Patseni mbale yatsopano ndipo muyikemo mchere." Ndipo anabweretsa mbaleyo kwa iye.
21 Kenaka Elisa anapita ku kasupe wa madziwo, nathiramo mchere mʼkasupemo nati, "Yehova akuti, ‘Ndachiritsa madzi awa. Madzi amenewa sadzabweretsanso imfa kapena kuchititsa kuti nthaka ikhale yosabereka.’ " 22 Kotero madziwo ndi abwino mpaka lero, molingana ndi mawu amene Elisa anayankhula.