Mafuta a Mkazi Wamasiye
1 Mkazi wa mmodzi mwa ana a aneneri anafuwula kwa Elisa kuti, "Mtumiki wanu, mwamuna wanga wamwalira ndipo inu mukudziwa kuti ankaopa Yehova. Koma tsopano munthu amene mwamuna wanga anakongolako zinthu zake, akubwera kudzatenga ana anga awiri aamuna kuti akhale akapolo ake."
2 Elisa anayankha mayiyo kuti, "Kodi ufuna ndikuchitire chiyani? Tandiwuza uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?"
Mayiyo anayankha kuti, "Mdzakazi wanu alibe kanthu kalikonse koma timafuta pangʼono chabe."
3 Elisa anati, "Pita kabwereke mitsuko yonse yopanda kanthu kwa anzako. Usakabwereke mitsuko yochepa. 4 Kenaka ukalowe mʼnyumba mwako ndi kudzitsekera iwe ndi ana ako. Mukakatero mukakhuthulire mafuta mʼmitsuko yonseyo, ndipo mtsuko uliwonse ukadzaza muzikawuyika pambali."
5 Mayi uja anachoka kwa Elisa nakadzitsekera ndi ana ake. Anthu anabweretsa mitsuko kwa iye ndipo ankathiramo mafuta. 6 Mitsuko yonse itadzaza, mayiyo anawuza mwana wake kuti, "Bweretsa mtsuko wina."
Koma iye anayankha kuti, "Mitsuko yonse yatha." Pamenepo mafuta analeka kutuluka.
7 Mayiyo anapita nakamuwuza munthu wa Mulungu amene anamuyankha kuti, "Pita, kagulitse mafutawo ndipo ukabweze ngongole ija. Ndalama zotsalazo zikakhale zako ndi ana ako."