Pular para o conteúdo
Publicidade

2 Reis 5

Naamani Achiritsidwa Khate Lake

1 Tsono Naamani anali mtsogoleri wa gulu lankhondo a mfumu ya ku Aramu. Iye anali munthu wodalirika pamaso pa mbuye wake ndipo anali wokondedwa kwambiri, chifukwa kudzera mwa iye Yehova anapambanitsa Aaramu. Anali msilikali wolimba mtima, koma anali ndi khate.

2 Tsono magulu a Aaramu anapita ku nkhondo ndipo anakagwira ukapolo mtsikana wamngʼono wa ku Israeli, ndipo ankatumikira mkazi wa Naamani. 3 Mtsikanayo anawuza mkazi wa Naamani kuti, "Mbuye wanga akanapita kukaonana ndi mneneri amene amakhala ku Samariya, akanachiritsidwa khate lawo."

4 Naamani anapita kwa mbuye wake kukamuwuza zomwe mtsikana wochokera ku Israeli ananena. 5 Mfumu ya ku Aramu inayankha kuti, "Iwe uyenera kupita. Ine ndilembera kalata mfumu ya ku Israeli." Choncho Naamani ananyamuka kupita ku Samariya, atatenga ndalama za siliva 30,000, ndalama zagolide 6,000 ndiponso zovala khumi za pa chikondwerero. 6 Kalata imene anapita nayo kwa mfumu ya ku Israeli inali ndi mawu awa: "Taonani, ndikutumiza Naamani mtumiki wanga pamodzi ndi kalatayi kwa inu kuti mumuchiritse khate lake."

7 Mfumu ya ku Israeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba mkanjo wake ndipo inati, "Kodi ine ndine Mulungu? Kodi ndingathe kupha kapena kupereka moyo? Chifukwa chiyani munthu ameneyu wanditumizira munthu woti ndimuchiritse khate lake? Taonani, iyeyu akungofuna kuti apeze chifukwa choyambanirana nane!"

8 Elisa munthu wa Mulungu atamva kuti mfumu ya ku Israeli yangʼamba mkanjo wake, anatumiza uthenga uwu: "Chifukwa chiyani mwangʼamba mkanjo wanu? Mutumizeni munthuyo kwa ine ndipo iyeyo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israeli." 9 Choncho Naamani anapita pamodzi ndi akavalo ake ndi magaleta nakayima pa khomo la nyumba ya Elisa. 10 Elisa anatumiza uthenga kwa iye woti, "Pita, kasambe kasanu ndi kawiri mu mtsinje wa Yorodani, thupi lako lidzachira ndi kukhalanso monga kale ndipo udzayeretsedwa."

11 Koma Naamani anachoka mokwiya ndipo anati, "Ine ndimaganiza kuti munthuyu atuluka ndipo ayimirira nayitana dzina la Yehova Mulungu wake, nayendetsa dzanja lake pamwamba pa nthendayi ndi kundichiritsa khate langa. 12 Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siyoposa mitsinje ina yonse ya ku Israeli? Kodi sindikanasamba mʼmitsinje imeneyo ndi kuyeretsedwa?" Kotero anatembenuka nachoka ali wokwiya kwambiri.

13 Antchito ake anamuyandikira namufunsa kuti, "Abambo anga, mneneri akanakulamulani chinthu chachikulu, kodi inu simukanachita? Nanga nʼzovuta motani zomwe mneneri wanena kuti Kasambeni ndipo mudzayeretsedwa!’ " 14 Choncho Naamani anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata.

Veja também