Pular para o conteúdo
Publicidade

2 Reis 6

Nkhwangwa Iyandama pa madzi

1 Ana a aneneri anati kwa Elisa, "Taonani malo amene timakhala ndi inu atichepera kwambiri. 2 Tiloleni tipite ku Yorodani kumene aliyense wa ife akadule mtengo umodzi, kuti timange malo woti tizikhalamo."

Ndipo Elisa anati, "Pitani."

3 Mmodzi wa iwo anati, "Chonde mulole kutsagana nawo atumiki anu."

Elisa anayankha kuti, "Ndipita nanu." 4 Ndipo anapita nawo.

Anapita ku Yorodani nayamba kudula mitengo. 5 Pamene wina ankadula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka nigwera mʼmadzi. Iye anafuwula kuti, "Mayo! Mbuye wanga! Popeza ndi yobwereka!"

6 Ndipo munthu wa Mulungu uja anafunsa, "Yagwera pati?" Pamene anamuonetsa malowo, Elisa anadula kamtengo nakaponya pamenepo, ndipo nkhwangwayo inayandama. 7 Elisa anati, "Itenge." Ndipo munthuyo anatambalitsa dzanja lake nayitenga.

Veja também