Pular para o conteúdo
Publicidade

2 SAMUELI 5

Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli

1 Mafuko onse a Israeli anabwera kwa Davide ku Hebroni ndipo anati, "Ife ndife mafupa ndi mnofu wanu. 2 Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ "

3 Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, mfumu inachita nawo pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli.

Veja também