Chilimbikitso Pokhala Wokhulupirika
3 Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga. 4 Ndikamakumbukira misozi yako, ndimalakalaka nditakuona kuti ndidzazidwe ndi chimwemwe. 5 Ndakumbukira za chikhulupiriro chako choona chimene chinayamba mwa agogo ako a Loisi ndi mwa amayi ako Yunike ndipo ndikutsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe.