21 "Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza;
sindikondwera nayo misonkhano yanu.
22 Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya,
Ine sindidzazilandira.
Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano,
Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.
23 Musandisokose nazo nyimbo zanu!
Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.
24 Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi,
chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!