10 Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga, 11 amene anati, "Lemba mʼbuku zimene ukuziona ndipo uzitumize ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Efeso, Simurna, Pergamo, Tiyatira, Sarde, Filadefiya ndi ku Laodikaya."