Pular para o conteúdo
Publicidade

CHIVUMBULUTSO 14

Mwana Wankhosa ndi Anthu 144,000

1 Kenaka ndinaona patsogolo panga panali Mwana Wankhosa, atayimirira pa Phiri la Ziyoni, ndipo Iye anali pamodzi ndi anthu 144,000 amene pa mphumi pawo panalembedwa dzina la Mwana Wankhosayo ndi la Atate ake. 2 Ndipo ndinamva liwu lochokera kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndinamvalo linali ngati a anthu akuyimba azeze awo. 3 Anthuwo ankayimba nyimbo yatsopano patsogolo pa mpando waufumu ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kuphunzira nyimboyo kupatula anthu 144,000 aja amene anawomboledwa pa dziko lapansi. 4 Awa ndiwo amene sanadzidetse koma anadzisunga ndipo sanadziyipitse ndi akazi. Anthu amenewa ndiwo ankatsatira Mwana Wankhosa kulikonse kumene ankapita. Ndiwo amene anagulidwa pakati pa anthu a dziko lapansi kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwana Wankhosa. 5 Iwo sananenepo bodza ndipo alibe cholakwa.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também