16 ‘Iwowa sadzamvanso njala,
sadzamvanso ludzu,
dzuwa kapena kutentha kulikonse
sikudzawawotcha.’
17 Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu
adzakhala mʼbusa wawo.
‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’
‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ "