Pular para o conteúdo
Publicidade

Machitidwe a Atumwi 12:5-12

5 Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu.

6 Usiku woti mmawa mwake Herode amuzenga mlandu, Petro amagona pakati pa asilikali awiri, atamangidwa maunyolo awiri, ndiponso alonda atayima pa khomo. 7 Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, "Fulumira, imirira!" Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro.

8 Kenaka mngelo anati kwa iye, "Vala zovala ndi nsapato." Ndipo Petro atachita izi mngeloyo anamuwuzanso kuti, "Funda chovala chako ndipo unditsate." 9 Petro anatsatira natuluka mʼndende, koma sanazindikire kuti zimene mngeloyo amachita zimachitikadi; iye amaganiza kuti amaona masomphenya. 10 Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka.

11 Pamenepo Petro anazindikira nati, "Tsopano ndikudziwa mosakayika kuti Ambuye anatuma mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode, ndi ku zoyipa zonse zimene Ayuda amafuna kundichitira."

12 Atazindikira zimenezi anapita ku nyumba ya Mariya amayi ake a Yohane, wotchedwanso Marko, kumene kunasonkhana anthu ambiri ndipo amapemphera.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.