Barnaba ndi Saulo Atumidwa ndi Mpingo
1 Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. 2 Iwo pamene ankapembedza Ambuye ndi kusala kudya, Mzimu Woyera anati, "Mundipatulire Barnaba ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndinawayitanira." 3 Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.