Paulo ndi Sila Mʼndende
16 Tsiku lina pamene timapita kumalo wopempherera, tinakumana ndi mtsikana wina amene anali ndi mzimu woyipa umene umanena zamʼtsogolo. Iye amapezera ndalama zambiri ambuye ake pa ulosi wake. 17 Mtsikanayu anatsatira Paulo ndi ife, akufuwula kuti, "Anthu awa ndi atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, amene akukuwuzani inu njira yachipulumutso." 18 Iye anachita izi masiku ambiri. Kenaka Paulo anavutika mu mtima, natembenuka ndipo anati kwa mzimuwo, "Ndikukulamula iwe mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye!" Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.