Pular para o conteúdo
Publicidade

Machitidwe a Atumwi 16:16-34

Paulo ndi Sila Mʼndende

16 Tsiku lina pamene timapita kumalo wopempherera, tinakumana ndi mtsikana wina amene anali ndi mzimu woyipa umene umanena zamʼtsogolo. Iye amapezera ndalama zambiri ambuye ake pa ulosi wake. 17 Mtsikanayu anatsatira Paulo ndi ife, akufuwula kuti, "Anthu awa ndi atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, amene akukuwuzani inu njira yachipulumutso." 18 Iye anachita izi masiku ambiri. Kenaka Paulo anavutika mu mtima, natembenuka ndipo anati kwa mzimuwo, "Ndikukulamula iwe mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye!" Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.

19 Pamene ambuye a mtsikana uja anazindikira kuti chiyembekezo chawo chopezera ndalama chatha, anagwira Paulo ndi Sila nawakokera ku bwalo la akulu. 20 Anawabweretsa iwo kwa oweruza milandu ndipo anati, "Anthu awa ndi Ayuda, iwo akuvutitsa mu mzinda wathu. 21 Ndipo akuphunzitsa miyambo imene ife Aroma sitiloledwa kuyilandira kapena kuyichita."

22 Gulu la anthu linatsutsana ndi Paulo ndi Sila, ndipo woweruza milandu analamula kuti avulidwe ndi kumenyedwa. 23 Atawakwapula kwambiri anawaponya mʼndende, nalamula woyangʼanira kuti awasunge mosamalitsa. 24 Chifukwa cha mawu amenewa woyangʼanira ndende anakawayika mʼchipinda chamʼkati mwa ndende, nawamangirira miyendo yawo mʼzigologolo.

25 Koma pakati pa usiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu, ndipo akayidi ena ankamvetsera. 26 Mwadzidzidzi kunachitika chivomerezi champhamvu kotero kuti maziko a ndende anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse za ndende zinatsekuka, ndipo maunyolo a aliyense anamasuka. 27 Woyangʼanira ndende uja atadzuka ku tulo, anaona kuti zitseko za ndende zinali zotsekula, ndipo anasolola lupanga lake nafuna kudzipha chifukwa ankaganiza kuti amʼndende athawa. 28 Koma Paulo anafuwula kuti, "Usadzipweteke! Tonse tilipo!"

29 Woyangʼanira ndendeyo anayitanitsa nyale, nathamangira mʼkati ndipo anadzigwetsa pa mapazi a Paulo ndi Sila akunjenjemera. 30 Iye anawatulutsa kunja ndipo anawafunsa kuti, "Amuna inu, ndichite chiyani kuti ndipulumuke?"

31 Iwo anayankha kuti, "Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako." 32 Kenaka analalikira mawu a Ambuye kwa iyeyo ndi onse amene anali mʼnyumba mwake. 33 Usiku womwewo woyangʼanira ndendeyo anawatenga nakawatsuka mabala awo; ndipo pomwepo iye ndi a mʼbanja lake anabatizidwa. 34 Woyangʼanira ndendeyo anapita nawo ku nyumba yake, nakawapatsa chakudya, ndipo banja lonse linadzazidwa ndi chimwemwe chifukwa anakhulupirira Mulungu.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.