Pular para o conteúdo
Publicidade

Atos 16

25 Koma pakati pa usiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu, ndipo akayidi ena ankamvetsera. 26 Mwadzidzidzi kunachitika chivomerezi champhamvu kotero kuti maziko a ndende anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse za ndende zinatsekuka, ndipo maunyolo a aliyense anamasuka. 27 Woyangʼanira ndende uja atadzuka ku tulo, anaona kuti zitseko za ndende zinali zotsekula, ndipo anasolola lupanga lake nafuna kudzipha chifukwa ankaganiza kuti amʼndende athawa. 28 Koma Paulo anafuwula kuti, "Usadzipweteke! Tonse tilipo!"

29 Woyangʼanira ndendeyo anayitanitsa nyale, nathamangira mʼkati ndipo anadzigwetsa pa mapazi a Paulo ndi Sila akunjenjemera. 30 Iye anawatulutsa kunja ndipo anawafunsa kuti, "Amuna inu, ndichite chiyani kuti ndipulumuke?"

31 Iwo anayankha kuti, "Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako." 32 Kenaka analalikira mawu a Ambuye kwa iyeyo ndi onse amene anali mʼnyumba mwake. 33 Usiku womwewo woyangʼanira ndendeyo anawatenga nakawatsuka mabala awo; ndipo pomwepo iye ndi a mʼbanja lake anabatizidwa. 34 Woyangʼanira ndendeyo anapita nawo ku nyumba yake, nakawapatsa chakudya, ndipo banja lonse linadzazidwa ndi chimwemwe chifukwa anakhulupirira Mulungu.

Veja também