Uthenga wa Petro
14 Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: "Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena. 15 Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa! 16 Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti:
17 " ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza
ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.
Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera,
anyamata anu adzaona masomphenya,
nkhalamba zanu zidzalota maloto.
18 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi,
ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo,
ndipo iwo adzanenera.
19 Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga
ndi zizindikiro pa dziko lapansi pano,
ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
20 Dzuwa lidzadetsedwa
ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi
lisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye.
21 Ndipo aliyense amene adzayitana
pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’
22 "Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa. 23 Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. 24 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa. 25 Pakuti Davide ananena za Iye kuti,
" ‘Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse.
Chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja,
Ine sindidzagwedezeka.
26 Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera;
thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo.
27 Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda,
kapena kulekerera Woyerayo kuti awole.
28 Inu munandidziwitsa ine njira zamoyo;
Inu mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
29 "Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino. 30 Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu. 31 Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole. 32 Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi. 33 Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi. 34 Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti,
" ‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti:
Khala kudzanja langa lamanja
35 mpaka nditasandutsa adani ako
kukhala chopondapo mapazi ako.’
36 "Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi."
37 Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, "Abale, kodi ife tichite chiyani?"
38 Petro anawayankha kuti, "Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. 39 Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane."
40 Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, "Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno." 41 Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo.