Hananiya ndi Safira
1 Koma munthu wina dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsanso munda wawo. 2 Mogwirizana ndi mkazi wakeyo anapatulapo pa ndalamazo nazisunga, ndipo anatenga zotsalazo ndi kukapereka kwa atumwi.
3 Koma Petro anamufunsa kuti, "Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama? 4 Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu."